KUGWIRA NTCHITO MODZIPEREKA (Commitment to Service)
2 Timoteo 2:1-6
“Iwe mwana wanga, ukhale olimbika muchisomo chopezeka mwa Yesu Khristu. Ndipo zomwe wazimva kuchokera kwa ine zochitira umboni uphunzitsenso kwa anthu ena odalirika omwenso ayenerezedwa kuphunzitsa ena. Ukhale opilira nafe m’mavuto ngati ankhondo ake a Yesu Khristu. Msilikali satanganidwanso ndi zinthu zakunja chifukwa amafuna kusangalatsa msilikali wamkulu. Chimodzimodzi ngati wina achita mpikisano, salandira mphotho mpakana atapambana molingana ndi malamulo a mpikisanowao” Mlimi olimbika ntchito ayenera ayenera kukhala oyambilira kulandira zokolora”.
Mafanizo Atatu a Paulo
1. ASILIKALI A YESU
Kukhala Opilira: Mapemphero a m’mawa, kusala kudya, kukhazikitsa ntchito zatsopano, kulimbikira ntchito ku sukulu za ubusa komanso kukonza mkachisi, kukhala odziletsa, kutumikira ngakhale mwadzidzidzi – zonsezi sizitipangitsa ife kukhala opambana, imeneyi ndiye ntchito yathu ngati asilikali. Tangoganizilani za msilikali wodzitamandira yekha chifukwa chochita bwino. Akhristu ambiri masiku ano amadzitamandira okha pa ntchito za moyo wao wa uzimu.
Usatanganidwe ndi Zinthu za Kunja: (zinthu za padziko zomwe timatanganidwa nazo nthawi zina zimatilepheretsa ife ngakhale kupita kukachisi kukapemphera, izi ndi zinthu monga ndale, komanso maubwezi ena omwe amatichotsa ife pamaso pa Ambuye wathu)
2. OPIKISANAWO AZITSIRIZA MOLINGANA NDI MALAMULO
- Chidule pa uzimu, timachimo tamseri zonsezi zimatilepheretsa ife kukhala ogonjetsa monga momwe umakhalira mpikisano wa mpira kapena masewera ena.
- Osadzimverera zofooka koposa kuzikonza kuti zinthu zikhale bwino
- Ambiri amafuna kuti atchuke ndiwo mu mpingo ndi maudindo popanda kukula kwenikweni mu uzimu, kudzipereka, kukhulupirika, komanso chiyero pa maso pa Mlengi.
- Tisamakhale odana ndi anthu ena pa zifukwa zopanda pake pomwe olephera tiri ifeyo.
3. MLIMI OLIMBIKIRA
- Omwe amalimibkiratu amalandira zotuta zochuluka kwa Ambuye, nakhala nawo mdalitso
- Iwo omwe agwira ntchito molimbika adzalindira mphotho zochuluka, pamene agwira ntchito mopambana
CHOYAMBIRIRA: Kodi ntchito imeneyi timagwirira ndani?
Yesaya 55:2
“Uwonongeranji ndalama zako pa zomwe siziri mkate, ndi mphamvu zako pa zomwe sizikhutitsa?”
Masalimo 127:2
“Kwachabe chabe umadzukirira m’mamawa nukhala mpaka mbembembe, kusakasaka chakudya – koma Ambuye amapereka tulo kwa iwo amene akonda.”
Mateyu 6:33
“Funafunani ufumu wake wa Mulungu, ndi chiyero chake, ndipo zonse zidzapatsidwa kwa inu”
Ndi zomvetsa chisoni kuti mtumiki yemwe akanatha kutumikira mkachisi awononge nthawi yake posakasak chuma cha dziko lapansi. Chuma cha mtengo wapatali chikutiyembekezera kumwamba kwa nthawi zonse kwa ife omwe tadzipereka kugwira ntchito yake pansi pano. Bwanji titangolingalira zothandiza ena ndi zomwe tiri nazo? bwanji nthawi yathu titaigwiritsa ntchito potumikira nayo Mulungu? Bwanji titayendera anthu ena mu mpingo? Izi ndi zinthu zomwe zimafunika. Tikatero Mulungu adzatidalitsa ndikusamalira zina zomwe ife timazisowa.