The main language of Malawi, parts of Zambia, parts of Zimbabwe, and parts of Mozambique. Approximately 10 million native speakers. Also called Chewa, Chinyanja, or Nyanja.
Luka Akulemba Za Moyo wa Yesu
Wolemekezeka Teophilo:
1.Ambiri ayeseyesa kupereka mbiri ya zinthu zomwe zidachitika pakati pathu pofuna kutsiriza ndondomeko ya Mulungu. 2. Zimene alemba ziri kugwirizana ndi zomwe taphunzira kuchokera kwa anthu amene adaona zinthu zikuchitika kuyambira pachiyambi. Iwonso adatumikira Mulungu pakuwauza anthu za Uthenga Wake. 3.Ine ndidachiphunzira ichi mosamalitsa kuyambira pachiyambi. Tsono ndinaganizira kuzilembera kwa inu mu njira ya dongosolo lenileni. 4.Ndidachita izi kuti inu mungathe kutsimikizira kuti zimene mwaphunzitsidwa ndi zoona.
Ufulu Ndi Thupi: (Freedom And The Flesh – Galatians 5 vs 13:15)
Galatians 5 vs 13:15 – “Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi chitirani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.
“Ufulu†ndi mau omwe amapezeka kwambiri mu Chipangano Chatsopano, koma ambiri samamvetsetsa tanthauzo lake ndi cholinga chake. Mau ngati awa amakhala ndi matanthauzo osiyanasiyana potengera ndi nkhani yake. Tiyerekeze ndi katundu ogulitsidwa monga “ulere†ngati palibe mtengo kapena mlingo. Tiyerekeze ndi dziko monga “mtendere†ngati kuli demokalase. Monga mwa zinthu zina zimakhala ndi matanthauzo ena.  Timagwiritsa ntchito mau nthawi zina ku chikhalidwe cha munthu chomwe sichobisika, kuseka momasuka, kulankhula momasuka (popanda zomuletsa).
Mwayamba kulamulira:Â Â Â Â Â (You Have Begun To Reign- Revelation 11 vs 17)
Revelation 11 vs 17:18 – “Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvu yonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru ndipo mwachita ufumuâ€.
“Mwadzitengera mphamvu yanu ndipo mwachita ufumu†– Izi kuunikira za chiphunzitso pomwe Akhristu ambiri amasokonezeka. “Ndi chiyani kusonyeza za nthawi ya kutsogolo pomwe Mulungu wa yamba kulandira?†anafunsa. Kodi Mulungu sakuchita kale ufumu? Kodi Mulungu sakulandira pa chirichonse? Alaliki amakonda kuuza anthu awo kuti Mulungu anatha kulandira pa chirichonse, koma kufotokozera kumeneku kumapangitsa anthu ena kukaikira ngati Mulungu alipodi makamaka akakumana ndi mavuto pano padziko. Baibulo likupereka mayankho ku mafunso ngati amenewa m’magawo ngati awa komanso Yohane oyamba 5 vs 19. Baibulo likuti Mulungu waika zonse pansi pa mapazi a Yesu (Aefeso 1 vs 22). continue
Chibvumbulutso 11 vs 17:18
“Nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, wamphamvu yonse, amene milu, nimunali, popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru, ndipo mwachita ufumu. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa akuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akuru; ndi kuononga iwo akuononga dziko.
Ambuye Mulungu Wamphamvu – Kumasulira mu Chigiriki mau akuti “Wamphamvu†apa ndi “Pantokratorâ€, nthawi yofunikira mu nthawi ya Chigiriki yake ya m’mamasulidwe a Chipangano Chakale. Zimachitika kupyolera m’buku la chibvumbulutso ndi mu Akorinto wachiwiri 6 vs 18, “Panto†kutanthauza kuti onse, “chirichonse†ndi “krator†kutanthauza “wamphamvuâ€. Mau anafikira magulu okhulupirira kwa okhulupirira oyambirira. Kutanthauza kuti mphamvu zonse m’Mwamba, kaya ndi mphamvu za ndale, kaya mphamvu za chibadwa, zikuchokera ndi kuperekedwa kuchokera mu mphamvu ya Mulungu. Ngati walora anthu ena kuti agwiritse mphamvu yake mongoyembekezera. continue
Tsiku La Pentekoste – gawo lachiwiri:       (The Day Of Pentecost part 2) – Acts 2 vs:12
“Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba nadzaza nyumba yonse imene anali kukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto, ndipo anakhala pa onse wayekha wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsaâ€.
“Koma anali m’Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu ulionse pansi pa thambo. Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana nusokonezedwa, popeza Yense anawamva alikulankhula chilankhulidwe chake cha iye yekha. Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa Sali Agalileya kodi? Ndipo nanga ife timva bwanji yense m’chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m’Mesopotamiya, m’Ponto, ndi m’Asiya; m’Frugiya, ndiponso m’Pafuliya, m’Aiguputo, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo ochokera ku Roma, ndiwo Ayuda ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m’malilime athu zazikuru za Mulungu. Ndipo anadabwa onse nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?
Phunziro lathali likufotokoza za mbiri ya Pentekoste, Chipembedzo cha Aisrayeli chinali masiku makumi asanu patatha m’Gonero. Phunziroli limalunjika pa zochitika za iwo eni zimene ziwonekera tsiku limenelo.
Anali onse pamodzi malo amodzi – kukumana limodzi mu umodzi ndipo pemphero ndiye chiyambi cha chokhacho cha kutsanuriridwa ndi chitsitsimutso mu mbiri. continue
Tsiku La Pentekoste Gawo Loyamba:  (The Day Of Pentecost part 1 – Acts 2 vs 1:12)
“Ndipo pakufika, tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. Ndipo mwadzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati nkokomo wa mphepo yolimba, nadzadza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.â€
“Koma anali m’Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo. Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva ali kulankhula m’chilankhulidwe chache cha iye yekha.â€
Tsiku la Pentekoste linali tsiku la phwando la Chiyuda limene a Israyeli anakhala akukondwerera kwa zaka zaka Khristu asanabwere. Mtundu wa chi Pentekoste umenewu, umagwirizana ndi kubadwa kwa mpingo, chiyambi cha Chikhristu monga kupita mtsogolo kusiyana ndi kungokhala ka gulu chabe ka ophunzira. Yesu adakonza za tsiku limeneli ndipo adauza ophunzira ake kudikira mu Yerusalemu kufikira zinthu izi zionekera (kuthiridwa kwa Mzimu Oyera).
Ndi Chifukwa Chiyani Yohane Anadyako Kabuku ? Chivumbulutso 10 vs 10:11 – (Why Did John Eat the Little Scroll ? Rev 10:10-11)
“Ndipo ndinatenga kabuku mdzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali mkamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m’mimba mwanga mudawawa. Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.â€
Kabuku kakang’ono – Mau a Mulungu; lero tiri nazo izi mu baibulo, ndi pamene Mzimu Oyera ayankhula, kaya mwachindunji ku mitima yathu, kapena kudzera mwa mavumbulutso mu msonkhano wa abale. Chizindikiro chimenechi chikuoneka mu Yesaya 29 vs 11:18 ndi Ezekieli 2 vs 9, 3 vs 4.
Kufunyulira buku m’manja mwa mngelo – Mulungu amapanga mau ake kukhala otseguka kwa onse. Ena amakana baibulo chifukwa amaona ngati losokoneza.
Lipenga La Chisanu Ndi Chiwiri – Chivumbulutso 11:15 (Revelation 11:15)
Chivumbulutso 11 vs 15 “Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba, ndipo panakhala mau akuru m’mwamba, ndikunena, ufumu wadziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wache, ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawiâ€.
Chivumbulutso 11 ndi theka chabe la bukuli, apa ndipomwe pamene Ambuye akutikumbutsa za komwe chirichonse chikulowera. Khristu wabwerera ndikulamulira nthawi zonse ndi iwo amene adziyeretsa kwa iwo okha kwa Iye.
M’ngelo wa chisanu ndi chiwiri – Monga kwafotokozeredwa mu phunziro lapitali, bukhu la Chivumbulutso liri ndi magawo anai. Chisanu ndi chiwiri ndi nambala yaphumphu yokwanira. Izo ndi makalata asanu ndi awiri kumpingo kuyamba buku, kutsatira ndi zotchingira zisanu ndi ziwiri zakumwamba, malipenga asanu ndi awiri, ndi mbale zofukizira ndi miriri isanu ndi iwiri. Zotchinga, malipenga ndi mbale zofukizira kukamba za zochitika.
Kulambira Kwa Akuru Makumi Awiri Ndi Mphambu Zinai – Chibvumbulutso 11:16
(Worship Of the Twenty four Elders: Revelation 11:16)
Chibvumbulutso 11 vs 16 – “Ndipo akuru makumi awiri ndi mphambu zinai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando ya chifumu yao, anagwa nkhope yao pansi, nalambira Mulungu…â€
Gawo limeneli likufotokoza za nyimbo ya kumwamba pamene ntchito ya Mulungu yatha  – pamene Yesu adzadza kudzakhazikitsa  mpando wake wachifumu padziko.  Ikutiphunzitsanso chiphunzitso chozama kwa Akhristu lero.
Akuru makumi awiri ndi mphambu zinai – Akuru makumi awiri ndi mphambu zinai akuwonekera m’buku lonse la Chivumbulutso. Amakhala pamipando yachifumu mozungulira mpando wa chifumu wa Mulungu kumwamba; atavala zovala zoyera ndi akorona agolide (Chivumbulutso 4 vs 4).
Choonadi Mukulambira – Yohane 4:23 ( Truth In Worship John 4:23)
Yohane 4 vs 23
“Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi mchoonadi; Pakuti Atate afuna otere akhale wolambira ache.
Cholinga chopembedza kwenikweni ndikufuna kusangalatsa Mulungu, osati kudzikondweretsa tokha. Ngati tifuna kumukondweretsa Mulungu tikuyenera kulambira motengera ndi chifuniro chake, mmene Iye watifunsira ife tichitire. Atsogoleri a chi Khristu akuyenera kumfunsa Ambuye mmene Iye akufunira kuti timulambire, ndikumupatsa Iye mwayi woti atiyankhule ndi kutitsogolera ife. Muli machaputala ambiri amene akukamba za mmene tingapembedzere kusiyana ndi momwe akukambira za momwe anachitira za chilengedwe cha dziko.