Ang Buluhaton sa Pagsulti batok sa Sayop nga Balita
(The Duty to Speak Up Against False Rumors)
Leviticus 5:1 – “Kon ang usa ka tawo magdumili sa pagsaksi bahin sa butang nga iyang nakita ug nasayran, makasala siya ug kinahanglan siyang silutan.”.
Ang Biblia nagtudlo nga aduna kita’y buluhaton paglihok, sa hustong mga butang. Sa daghang kahimtang, ang dili pagkibo makatampo sa delikadong sala. “Ang Matag-usa, nga nasayod sa husto niyang buhaton unya magdumili sa pagbuhat, kini sala.” (Santiago 4:17. Kadaghanan sa sistema legal sa kalibutan wala mo ila sa “Crime of omission”, gawas sa kasagaran nga kahimtang. Ang Biblia gayud – diin ang Dios naglaum sa pipila ka butang, ug ang dili paglihok sa tawo hulagway sa pagsupak.
KUKHALA CHOPHWEKA KOMA CHOYANG’ANITSITSA
1 Akorinto 1:17-23 – “Pakuti Khristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mawu, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe opanda pache. Pakuti mawu a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutaika, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu. …. koma ife talalikira Khritu wopachikidwa”
Tikuona mu vesi limeneli komanso vesi la m’mwamba kuchokera ku 1 Akorinto 2, Paulo sanasamale zosangalatsa anthu kapena kuonetsa chikhalidwe ngati wolalikira wa mkulu. Sanagwiritse ntchito mawu kuti anthu amve ngati iye ndi wamzeru, ngakhale iye anakatha kuzichita izi bwino koposa wina aliyense, kupatsidwa chidwi chake kuphunzira ndi chikhalidwe chake ngati ophunzira. Sanapereke zinthu zotiyenereza kukhala Mkhristu. Kalalikidwe kake kanali kosavuta komanso koyang’ana kwa Yesu. Iye anamvetsetsa kuti anthu akuyenera kukhala komanso kukumana ndi Yesu, kuphunzira za mphamvu ya mwazi wa Yesu komanso kuuka kwake. Pamene anthu adziwa zinthu zimenezi Mzimu oyera udzafika ndikuyamba kulamulira.
KULAKIRA KWA PAULO
1 Akorinto 2:2-4 “Ndipo mawu anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mawu okopa anzeru, koma m’chionetso cha Mzimu ndi champhamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma ya mu mphamvu ya Mulungu. ”
Pali mawu ena amene munthu wina otchuka, Augustine Hippo ananena. Iye anati: Pali zinthu zitatu zimene iye amafuna kuonetsetsa ndi maso ake, koma sanathe, “Ambuye Yesu mu nthawi ya utumiki wake padziko lapansi, wolamulira wamkulu wa ku Rome ndi kutchuka kwake ndi kulamulira kwa Paulo, momga olalikira opatsa chidwi komanso otchuka kwambiri, (ngati Augustine amene anali mphunzitsi waukachenjede asanasandulike) chifukwa Baibulo likutiuza zambiri za utumiki wake komanso zitsanzo zambiri mu malemba kuposa chiri chonse mu chipangano cha tsopano. Inde, tikuona kuti Mulungu anakhazikitsa Paulo ngati chitsanzo kuti Akhristu titsatire pophatikizirapo zitsanzo zambiri zimene zinali mu zolembera zake. Paulo monga olalikira woyamba, maganizo amene amakhala ndi anthu ambiri zimakhala zosiyana ndi zimene Baibulo likunena pa kulalikira kwake.
CHANGU CHA PAULO PAKUMVERA
Afilipo 2:5-7 “Mukhale nao mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu, ameneyo pokhala nao maonekedwe a Mulungu sanachiyese cholanda kukhala ofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha natenga maonekedwe a ukapolo, nakhala mafanizidwe a munthu, ”
1 Akorinto 11:1 “Khalani onditsanza ine monga m’mene nditsanza ndi Khristu. ”
M’madera ambiri amoyo wake, Paulo anakhazikitsa dongosolo la chikhakidwe chomwe samalimbana ndi okhulupirira ena amene amatsanzira. Kudalira ku mphamvu zimene Mzimu Woyera anamupatsa iye kukagonjetsa zofuna za thupi lake, Paulo analimbikira kumutsanza Yesu Khristu. Paulo anamvetsetsa mu zaka zimene Yesu anayenda ngati munthu pa dzik olapansi mu utumiki wake, anakanitsitsa kupanga kapena kuchita chiri chonse koma chokhacho chomwe chinamukondweretsa Tate wake. Mwa njira imeneyi, pamene Yesu anadzitengera yekha “chikhalidwe cha kapolo” anatipatsa ife chitsanzo chooneka bwino m’mene zingaonekere pakuyang’anira chindunji pa kutumikira Mulungu. Yesu anayankhula mawu okhawo ochokera kwa Atate. Anachita zinthu zokhazo zomwe zinamukondweretsa Atate, ndipo sanalore chikhalidwe cha umunthu wake kutsogolera zomwe akunena ndi kuchita.
KUDZIPEREKA KWA PAULO KU MUYAYA
Akolose 3:1-4 “Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani za kumwamba, kumene kuli Khristu okhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai. Pakuti munafa ndipo moyo wanu wabisika ndi Khristu mwa Mulungu. Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamene inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye m’ulemerero. ”
Chinthu chimodzi cha makalata amene Paulo amalemba amayang’ana pa muyaya. Anthu ambiri masiku ano amaganiza za mtumwi Paulo monga mphumzitsi wamkulu kapena kuti odzala mipingo kapenanso munthu amene anapanga zinthu zodabwitsa zazikulu. Zinthu zonsezi ndi zoona. Koma tikamamuona Paulo mwini, timuona kuti anayesesa kufuna kukhazikitsa moyo wake pa Khristu komanso kufuna umuyaya wa Mulungu.
MTHUNZI WA WAMPHAMVU YONSE Masalmo 91:1
“ Iye amene akhala pansi m’ngaka yace ya Wam’mwambamwamba, adzagonera mumthunzi wa Wamphanvu yonse”
Chigawo choyamba cha phunziroli, chikuyang’ana gawo loyamba la vesi limeneli, “Mthunzi wa Wam’mwambamwamba” ndipo chigawo chachiwiri chikuyang’ana mbali ina ya vesi lomweli. (Ndime imeneyi ili ndi magawo awiri omwe mawu ake akuchokera mu Chihebri. )
KUPUMA: Mawu oyamba mu chigawo choyamba cha vesili, “Kukhala” kulodzera chisankho chomwe tayenera kupanga- kukhala chifupi ndi Mulungu mu thupi lake ndi muvumbulutso.

KULIKANIKIZA KHUTU NDI CHITSEKO: (Thrust his ear through the door)
Deutronomo 15:16-17 - “Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu, pamenepa muzitenga lisungulo, ndikulipisa mkhutu mwache, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu”
Izi zikukamba za atumiki komanso akapolo mu chipangano chakale, koma kufotokozera m’mene tikukhalira atumiki a Ambuye masiku ano. Pali goli lofanana ndi dongosolo lache pa Eksodo 21:2-6. Aisraeli amayenera kumasula kapolo wawo wa chiHebri kapena mtumiki wina aliyense akagwira ntchito kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Ngakhale zinali chonchi, atumiki amakhalabe mu udindowo mokhazikika ngati anafuna kutero. Chiyankhulo cheni cheni cha Baibulo sichinasiyanitse pakati pa kapolo ndi mtumiki monga timachitira mu chingerezi.
BULU NDI CHOIKAPO CHAKE (Donkey and the Saddle)
Marko 11:1-7, Matt. 21
“Ndipo anati kwa iwo, pitani pa mudzi wa pandunji nanu; mukangolowa m’menemo mudzapeza mwana wa bulu.”
KUDIKIRA NGONGOLE (CHIKOLE)
“Mukakongoletsa mnasi wanu ngongole iri yonse, musamalowe nyumba mwake kudzitengera chikole chake. Muima pa bwalo, ndi munthu amene amkongoletsayo adzituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo. ”
CHIYAMBI: Monga gawo limene lafotokozedwa kuti wobwereketsa akuyenera kudikira pakhomo pa yemwe wabwerekayo, chomwecho chipangano chatsopano chikuti Yesu akudikira pa khomo la miyoyo yathu, kudikirira ife. “Ine ndiri pano! Ndaima pakhomo ndipo ndigogoda. ” Chivumbulutso 3:20. Ichi ndi chikonzero cha chinenero chomwe ife ochimwa tikuyenera kulumikizana ndi Yesu polandira cholowa cha chipulumutso chake. Yesu ndi amene ali ndi chiri chinso chomwe tifuna- chikhululukiro kumachimo, kubadwa mwatsopano, vumbulutso la Mzimu Woyera, mphatso za Mzimu, kuyeretsa komanso zina zambiri. Timabwera kwa Iye pamene tikufuna chiri chonse. Mwatokha, mu thupi lathu, palibe china chiri chonse chimene timafuna kwa muyaya.
ANG ULO SA IGLESIA (The Head of the Church)
Colosas 1:18
Siya mao ang ulo sa lawas, ang Iglesia: nga mao ang sinugdanan, ang inunahang bunga gikan sa mga patay: nga sa tanang butang siya ang kinalabwan.